13 Gidiyoni atafika kumsasawo, anamva wina akufotokozera mnzake zimene analota kuti: “Tamvera zimene ndalota ine. Ndalota mkate wa balere wozungulira ukugubuduzika kubwera mumsasa wa Amidiyani. Mkatewo unafika nʼkuwomba tenti ina moti tentiyo inagwa.+ Mkatewo unagadabuza tentiyo mpaka kuphwasuka.”