15 Ndiyeno pa tsiku lachinayi anayamba kuuza mkazi wa Samisoni kuti: “Umunyengerere mwamuna wako kuti atiuze tanthauzo la mwambiwu.+ Akapanda kutiuza, tikutentha ndi moto pamodzi ndi nyumba ya bambo ako.+ Kodi anthu inu mwatiitana kuti mutilande katundu wathu?”+