16 Pamenepo mkazi wa Samisoni anayamba kulira pamaso pa mwamuna wake,+ ndipo ankamuuza kuti: “Umandida, sundikonda ayi.+ Iwe waphera mwambi anthu a mtundu wanga,+ koma ine sunandiuze tanthauzo lake.” Atatero anamuuza kuti: “Ndikuuze chifukwa chiyani, pamene bambo kapena mayi anga sindinawauze?”+