-
2 Samueli 12:20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Davide atamva zimenezi anadzuka pansi pamene anagonapo n’kukasamba ndi kudzola+ mafuta. Kenako anasintha zovala zake n’kukalowa m’nyumba+ ya Yehova ndipo anagwada n’kuweramira pansi.+ Atachoka kumeneko anakalowa m’nyumba yake ndi kupempha kuti amukonzere chakudya. Mwamsanga anam’bweretsera mkate ndipo anadya.
-
-
2 Samueli 14:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Choncho Yowabu anatumiza anthu ku Tekowa+ kuti akatenge mkazi wanzeru.+ Atabwera naye, Yowabu anamuuza kuti: “Chonde ukhale ngati munthu amene ali panyengo yolira maliro, ndipo uvale zovala za panyengo yolira maliro, komanso usadzole mafuta.+ Ukatero ukhale ngati mkazi amene wakhala akulira maliro kwa masiku ambiri.+
-