25 Kenako Yehova anatsika mumtambo+ n’kulankhula naye.+ Anatengako gawo lina la mzimu+ umene unali pa Mose n’kuuika pa aliyense wa akulu 70 amenewo. Ndipo mzimuwo utangokhala pa iwo, anayamba kuchita zinthu ngati aneneri, koma sanadzachitenso kachiwiri.+