2 pa nthawi imeneyo Yehova analankhula kudzera mwa Yesaya mwana wa Amozi,+ kuti: “Pita+ ukavule chiguduli chimene chili m’chiuno mwako+ ndipo ukavulenso nsapato zimene zili kuphazi kwako.”+ Iye anakachitadi zimenezo, n’kumayenda wopanda zovala ndiponso wopanda nsapato.+