11 Ndiyeno onse amene anali kumudziwa atamuona, anadabwa kuona kuti ali pakati pa aneneri ndipo akulankhula ngati mneneri. Choncho anthuwo anayamba kufunsana kuti: “Kodi chachitikira mwana wa Kisi n’chiyani? Kodi Sauli nayenso ndi mmodzi wa aneneri?”+