13 Nthawi yomweyo Davide ananyamuka pamodzi ndi amuna pafupifupi 600+ amene anali kuyenda naye. Iwo anatuluka mu Keila ndi kumangoyendayenda kulikonse kumene akufuna. Ndiyeno uthenga unafika kwa Sauli kuti Davide wathawa ku Keila. Sauli atamva zimenezi sanapitekonso.