-
1 Samueli 6:4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Ndiyeno iwo anafunsa kuti: “Kodi nsembe ya kupalamula imene tiyenera kupereka ikhale chiyani?” Poyankha, ansembe ndi alauli aja anati: “Mupereke zifanizo zisanu zagolide za matenda a mudzi, ndi zifanizo zisanu zagolide za mbewa zoyenda modumpha, malinga ndi chiwerengero cha olamulira ogwirizana+ a Afilisiti. Muchite zimenezi pakuti mliri umene wagwera aliyense wa inu, pamodzi ndi olamulira anu ogwirizana ndi umodzi.
-