20 Azichita zimenezi kuti mtima wake usadzikweze pamaso pa abale ake,+ komanso kuti asachoke pachilamulo mwa kupatukira kudzanja lamanja kapena lamanzere.+ Azichita zimenezi kuti iyeyo ndi ana ake atalikitse masiku a ufumu wawo+ mu Isiraeli.
28 Zitatero, Samueli anamuuza kuti: “Yehova wang’amba+ ndi kuchotsa ufumu wa Isiraeli kwa iwe lero, ndipo adzaupereka kwa mnzako, munthu woyenerera kuposa iwe.+