4 Tsopano pakati pa mipata imene Yonatani anafuna kudutsa kuti akamenyane ndi mudzi wa asilikali+ a Afilisiti, panali thanthwe looneka ngati dzino kumbali ina, ndi lina looneka ngati dzino kumbali inanso. Limodzi mwa matanthwewo dzina lake linali Bozezi ndipo linalo linali Sene.