22 Benaya+ mwana wa Yehoyada,+ mwana wa munthu wolimba mtima, anachita zinthu zambiri ku Kabizeeli.+ Iye anapha ana awiri a Ariyeli wa ku Mowabu, ndipo analowanso m’chitsime chopanda madzi n’kupha mkango+ umene unali m’chitsimemo pa tsiku limene kunagwa chipale chofewa.