12 Anthu a m’dziko lonselo adzalira mokuwa.+ Banja lililonse lizidzalira palokha. Banja la nyumba ya Davide lizidzalira palokha, ndipo akazi a m’banja limeneli azidzalira paokha.+ Banja la nyumba ya Natani+ lizidzalira palokha, ndipo akazi a m’banja limeneli azidzalira paokha.