Levitiko 15:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 “‘Mwamuna akatulutsa umuna,+ azisamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo. Deuteronomo 23:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 “Ukamanga msasa kuti umenyane ndi adani ako, uzidzipatula ku choipa chilichonse.+ 1 Samueli 21:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Davide anayankha wansembeyo kuti: “Koma akazi sanatiyandikire monga mmene zinakhaliranso poyamba pamene ndinapita kukamenya nkhondo.+ Anyamatawo amakhala oyera ngakhale pamene tili pa ntchito wamba. Ndiye kuli bwanji lero pamene tili pa ntchito yapadera?”
5 Davide anayankha wansembeyo kuti: “Koma akazi sanatiyandikire monga mmene zinakhaliranso poyamba pamene ndinapita kukamenya nkhondo.+ Anyamatawo amakhala oyera ngakhale pamene tili pa ntchito wamba. Ndiye kuli bwanji lero pamene tili pa ntchito yapadera?”