14 “Yairi+ mwana wamwamuna wa Manase anatenga dera lonse la Arigobi+ mpaka kumalire a Agesuri+ ndi a Amaakati,+ ndipo midzi ya ku Basana imeneyo anaitcha dzina la iye mwini lakuti, Havoti-yairi*+ kufikira lero.
3 Mwana wake wachiwiri anali Kileyabu+ wobadwa kwa Abigayeli+ wa ku Karimeli, amene anali mkazi wa Nabala, ndipo wachitatu anali Abisalomu+ wobadwa kwa Maaka, mwana wamkazi wa Talimai+ mfumu ya ku Gesuri.
37 Koma Abisalomu anathawa ndi kupita kwa Talimai,+ mfumu ya dziko la Gesuri,+ amene anali mwana wamwamuna wa Amihudi. Davide anali kulira+ tsiku ndi tsiku chifukwa cha imfa ya Aminoni mwana wake.