33 Pamenepo mfumu inasokonezeka ndipo inakwera m’chipinda cha padenga+ cha pachipata ndi kuyamba kulira. Mfumu inali kuyenda n’kumanena kuti: “Mwana wanga Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga+ Abisalomu! Haa! Zikanakhala bwino ndikanafa ndine m’malo mwa iwe, Abisalomu mwana wanga, mwana wanga!”+