31 Koma Yowasi+ anauza onse amene anamuukirawo kuti:+ “Kodi inu mungaweruzire Baala mlandu kuti mum’pulumutse? Aliyense womuweruzira mlandu ayenera kuphedwa m’mawa womwe uno.+ Ngati Baalayo ndi Mulungu,+ adziweruzire yekha mlanduwu,+ chifukwa wina wake wagwetsa guwa lake lansembe.”