Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Mafumu 18:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Choncho anatenga ng’ombe yaing’ono yamphongo imene Eliya anawapatsa, n’kuikonza. Kenako anayamba kuitana dzina la Baala kuyambira m’mawa mpaka masana. Ankaitana kuti: “Inu a Baala, tiyankheni!” Koma sipanamveke mawu alionse,+ ndipo palibe anayankha.+ Iwo anapitiriza kudumphadumpha ngati akuvina, kuzungulira guwa lansembe limene anamanga.

  • 1 Mafumu 18:39
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 39 Anthu onsewo ataona zimenezo, nthawi yomweyo anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi,+ ndipo ananena kuti: “Yehova ndiye Mulungu woona! Yehova ndiye Mulungu woona!”

  • Yesaya 41:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Nenani zinthu zimene zikubwera m’tsogolo, kuti tidziwe kuti inu ndinu milungu.+ Inde, muyenera kuchita zabwino kapena zoipa, kuti tizionere limodzi ndi kuchita mantha.+

  • Yeremiya 10:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Ali ngati choopsezera mbalame m’munda wa minkhaka ndipo sangalankhule.+ Iwo amachita kunyamulidwa ndithu chifukwa sangathe kuyenda okha.+ Mafano musamachite nawo mantha chifukwa sangakuvulazeni, ndipo kuwonjezera pamenepo, sangachite chabwino chilichonse.”+

  • 1 Akorinto 8:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ndiyeno pa nkhani ya kudya+ zakudya zoperekedwa kwa mafano, timadziwa kuti fano ndi lopanda pake+ m’dziko, ndiponso kuti kulibe Mulungu wina koma mmodzi yekha.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena