Yesaya 41:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Nenani zinthu zimene zikubwera m’tsogolo, kuti tidziwe kuti inu ndinu milungu.+ Inde, muyenera kuchita zabwino kapena zoipa, kuti tizionere limodzi ndi kuchita mantha.+ Yesaya 44:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Anthu onse opanga zifaniziro zosema ndi opanda pake,+ ndipo mafano awo okondedwa adzakhala opanda phindu.+ Monga mboni zawo, mafanowo saona chilichonse ndipo sadziwa chilichonse,+ kuti anthu opanga mafanowo achite manyazi.+ Yesaya 45:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 “Sonkhanani pamodzi n’kubwera kwa ine.+ Unjikanani pamodzi, inu anthu opulumuka ku mitundu ya anthu.+ Amene amanyamula chifaniziro chawo chosema chamtengo sadziwa kanthu, mofanana ndi amene amapemphera kwa mulungu woti sangawapulumutse.+ 1 Akorinto 8:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Ndiyeno pa nkhani ya kudya+ zakudya zoperekedwa kwa mafano, timadziwa kuti fano ndi lopanda pake+ m’dziko, ndiponso kuti kulibe Mulungu wina koma mmodzi yekha.+
23 Nenani zinthu zimene zikubwera m’tsogolo, kuti tidziwe kuti inu ndinu milungu.+ Inde, muyenera kuchita zabwino kapena zoipa, kuti tizionere limodzi ndi kuchita mantha.+
9 Anthu onse opanga zifaniziro zosema ndi opanda pake,+ ndipo mafano awo okondedwa adzakhala opanda phindu.+ Monga mboni zawo, mafanowo saona chilichonse ndipo sadziwa chilichonse,+ kuti anthu opanga mafanowo achite manyazi.+
20 “Sonkhanani pamodzi n’kubwera kwa ine.+ Unjikanani pamodzi, inu anthu opulumuka ku mitundu ya anthu.+ Amene amanyamula chifaniziro chawo chosema chamtengo sadziwa kanthu, mofanana ndi amene amapemphera kwa mulungu woti sangawapulumutse.+
4 Ndiyeno pa nkhani ya kudya+ zakudya zoperekedwa kwa mafano, timadziwa kuti fano ndi lopanda pake+ m’dziko, ndiponso kuti kulibe Mulungu wina koma mmodzi yekha.+