1 Akorinto
8 Tsopano ponena za zakudya zoperekedwa kwa mafano,+ tikudziwa kuti tonse ndife odziwa zinthu.+ Kudziwa zinthu kumachititsa munthu kudzitukumula, koma chikondi chimamangirira.+ 2 Ngati wina akuganiza kuti akudziwa za chinachake,+ sanachidziwebe mokwanira.+ 3 Koma ngati munthu akukonda Mulungu,+ ameneyo amadziwika kwa Mulungu.+
4 Ndiyeno pa nkhani ya kudya+ zakudya zoperekedwa kwa mafano, timadziwa kuti fano ndi lopanda pake+ m’dziko, ndiponso kuti kulibe Mulungu wina koma mmodzi yekha.+ 5 Pakuti ngakhale ilipo yotchedwa “milungu,”+ kaya kumwamba+ kapena padziko lapansi,+ ndipo n’zoona ilipodi “milungu” yambiri ndi “ambuye” ambiri,+ 6 kwa ife Mulungu alipo mmodzi yekha basi+ amene ndi Atate.+ Iye ndi amene zinthu zonse zinachokera mwa iye, ndipo ifeyo ndife ake.+ Ndipo pali Ambuye+ mmodzi, Yesu Khristu,+ amene zinthu zonse zinakhalapo kudzera mwa iye,+ ndipo ifeyo kudzera mwa iyeyo.
7 Ngakhale zili choncho, si onse amene amadziwa zimenezi.+ Koma ena, pokhala ozolowera mafano enaake mpaka panopo, akamadya chakudya choperekedwa kwa fano amachidya monga choperekedwadi kwa fano,+ ndipo popeza chikumbumtima chawo n’chofooka, chimaipitsidwa.+ 8 Koma chakudya sichingatikometse pamaso pa Mulungu.+ Ngati sitinadye chakudyacho, sikuti tamulakwira, ndiponso ngati tadya, sikuti tamukondweretsa mwapadera.+ 9 Koma muzikhalabe osamala kuti ufulu wanuwo usakhale chopunthwitsa kwa ofooka.+ 10 Pakuti ngati wina angaone iweyo wodziwa zinthuwe ukudya chakudya m’kachisi wa mafano, kodi chikumbumtima cha munthu wofooka uja sichidzamulimbikitsa kudya zakudya zoperekedwa kwa mafano?+ 11 Zikatero, ungawononge munthu wofookayo, yemwe ndi m’bale wako amene Khristu anamufera,+ chifukwa chakuti ukudziwa zinthu. 12 Koma inu mukamachimwira abale anu motero ndi kuvulaza chikumbumtima chawo+ chofookacho, mukuchimwira Khristu. 13 Chotero ngati chakudya chikukhumudwitsa+ m’bale wanga, sindidzadyanso nyama m’pang’ono pomwe, kuti ndisakhumudwitse m’bale wanga.+