Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 115:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Pakamwa ali napo koma salankhula,+

      Maso ali nawo koma saona.+

  • Salimo 135:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Pakamwa ali napo koma salankhula.+

      Maso ali nawo koma saona.+

  • Yesaya 44:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Iwo sadziwa chilichonse+ ndipo samvetsetsa chilichonse+ chifukwa maso awo amatidwa kuti asamaone,+ ndipo mitima yawo ndi yosazindikira zinthu.+

  • Yesaya 45:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 “Sonkhanani pamodzi n’kubwera kwa ine.+ Unjikanani pamodzi, inu anthu opulumuka ku mitundu ya anthu.+ Amene amanyamula chifaniziro chawo chosema chamtengo sadziwa kanthu, mofanana ndi amene amapemphera kwa mulungu woti sangawapulumutse.+

  • Yeremiya 10:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Ali ngati choopsezera mbalame m’munda wa minkhaka ndipo sangalankhule.+ Iwo amachita kunyamulidwa ndithu chifukwa sangathe kuyenda okha.+ Mafano musamachite nawo mantha chifukwa sangakuvulazeni, ndipo kuwonjezera pamenepo, sangachite chabwino chilichonse.”+

  • Danieli 5:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Mwadzikweza pamaso pa Ambuye wakumwamba+ ndipo anthu akubweretserani ziwiya za m’nyumba yake.+ Inuyo, nduna zanu, adzakazi anu ndi akazi anu ena apambali mwamwera vinyo m’ziwiya zimenezi. Mwatamanda milungu wamba yasiliva, yagolide, yamkuwa, yachitsulo, yamitengo ndi yamiyala+ imene siona, kumva kapena kudziwa kalikonse.+ Koma Mulungu amene amasunga mpweya wanu+ ndi njira zanu zonse m’dzanja lake,+ simunamulemekeze.+

  • Habakuku 2:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Kodi chifaniziro chosema, chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula ndiponso mphunzitsi wonama,+ zili ndi phindu lanji+ kuti wozipanga azizikhulupirira+ ndipo azipanga milungu yopanda pake yosalankhula?+

  • 1 Akorinto 8:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ndiyeno pa nkhani ya kudya+ zakudya zoperekedwa kwa mafano, timadziwa kuti fano ndi lopanda pake+ m’dziko, ndiponso kuti kulibe Mulungu wina koma mmodzi yekha.+

  • 1 Akorinto 10:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Ndiye ndinene chiyani? Kuti choperekedwa nsembe kwa fano chili kanthu, kapena kuti fanolo ndi kanthu?+

  • 1 Akorinto 12:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Mukudziwa kuti pamene munali a mitundu ina,+ munali kutsogoleredwa m’njira zosiyanasiyana ku mafano+ osalankhula.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena