Habakuku
2 Ine ndidzaimabe+ pamalo a mlonda ndiponso pakhoma lachitetezo. Ndidzakhala tcheru+ kuti ndione uthenga umene iye adzalankhula kudzera mwa ine+ ndi zimene ndidzayankha pamene iye akundidzudzula.+
2 Pamenepo Yehova anandiyankha kuti: “Lemba masomphenyawa moonekera bwino pamiyala yosema,+ kuti wowerenga mokweza awerenge mosadodoma.+ 3 Uchite zimenezi pakuti masomphenyawa akuyembekezera nthawi yake yoikidwiratu+ ndipo akuthamangira kumapeto kwake. Zimene zili m’masomphenyazi si zonama. Ngakhale masomphenyawa atazengereza, uziwayembekezerabe* chifukwa adzakwaniritsidwa ndithu.+ Iwo sadzachedwa.
4 “Taona! Iye wadzitukumula+ ndipo si wowongoka mtima. Koma wolungama adzakhalabe ndi moyo mwa chikhulupiriro chake.+ 5 Ndiye pakuti vinyo ndi wachinyengo,+ mwamuna wamphamvu amadzimva,+ koma sadzakwaniritsa cholinga chake.+ Iye wakulitsa chilakolako chake ngati Manda* ndipo sangakhutire ngati imfa.+ Iye akupitiriza kudzisonkhanitsira mitundu yonse ya anthu ndi anthu onse pamodzi.+ 6 Kodi anthu onsewa sadzamunenera mwambi,+ chining’a ndi mawu okuluwika? Wina adzanena kuti,
“‘Kodi iye adzapitiriza kuchulukitsa zinthu zimene si zake+ kwa nthawi yaitali bwanji?+ Tsoka kwa iye pakuti akungochulukitsa ngongole yake. 7 Kodi amene uli nawo ngongole sadzanyamuka ndi kubwera modzidzimutsa kuti uwabwezere ngongole yawo? Kodi okugwedeza mwachiwawa sadzanyamuka ndi kubwera kudzafunkha zinthu zako zonse?+ 8 Chifukwa chakuti iwe unafunkha mitundu yambiri ya anthu, anthu onse otsala a m’mitunduyo adzafunkha zinthu zako.+ Iwo adzateronso chifukwa unakhetsa magazi a mtundu wa anthu komanso unachitira chiwawa dziko lapansi, tauni ndi anthu onse okhala mmenemo.+
9 “‘Tsoka kwa munthu amene akupezera nyumba yake phindu mwachinyengo.+ Iye akuchita zimenezi kuti amange chisa chake pamalo okwezeka ndi cholinga choti tsoka lisamupeze.+ 10 Wapereka malangizo ochititsa manyazi kunyumba yako, kumene ndi kuphetsa mitundu yambiri ya anthu+ ndipo wachimwa.+ 11 Mwala wa pakhoma* udzalira mwachisoni ndipo kuchokera padenga* mtanda wa denga udzayankha.+
12 “‘Tsoka kwa munthu amene akumanga mzinda mwa kukhetsa magazi, amenenso wakhazikitsa tauni mwa kuchita zosalungama.+ 13 Taona! Kodi si Yehova wa makamu amene adzachititsa anthu kugwira ntchito yakalavulagaga kuti moto uwononge ntchitoyo? Kodi sindiye amene wachititsa kuti mitundu ya anthu idzitopetse pachabe?+ 14 Pakuti dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa ulemerero wa Yehova ngati mmene madzi amadzazira nyanja.+
15 “‘Tsoka kwa amene akupatsa anzake chakumwa kuti amwe, koma atachisakaniza ndi mkwiyo ndiponso kupsa mtima kuti anzakewo aledzere+ ndipo iye aone maliseche awo.+ 16 Iwenso adzakumwetsa+ ndipo udzaonekera kuti ndiwe wosadulidwa.+ Udzakhuta zinthu zamanyazi m’malo mwa ulemerero.+ Chikho chochokera m’dzanja lamanja la Yehova chidzakupeza+ ndipo ulemerero wako udzasanduka manyazi. 17 Zidzakhala choncho chifukwa chiwawa chimene unachitira Lebanoni+ chidzafika pa iwe ndiponso chifukwa cha kuwononga kwako kwakukulu kumene unaopseza nako zilombo zakutchire, kukhetsa magazi a anthu ndi chiwawa chimene unachitira dziko lapansi,+ tauni ndi onse okhala mmenemo.+ 18 Kodi chifaniziro chosema, chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula ndiponso mphunzitsi wonama,+ zili ndi phindu lanji+ kuti wozipanga azizikhulupirira+ ndipo azipanga milungu yopanda pake yosalankhula?+
19 “‘Tsoka kwa munthu amene akuuza chidutswa cha mtengo kuti: “Dzuka!” Amene amauzanso mwala wosalankhula kuti: “Dzuka! Tipatse malangizo”!+ Taona! Fanolo ndi lokutidwa ndi golide ndi siliva+ ndipo mulibe mpweya* mkati mwake.+ 20 Koma Yehova ali m’kachisi wake wopatulika.+ Inu anthu onse a padziko lapansi, khalani chete pamaso pake!’”+