17 Chiwawa chimene unachitira Lebanoni chidzafika pa iwe.
Ndipo chiwonongeko chimene chinaopseza nyama zakutchire chidzabwera kwa iwe.
Chifukwa unakhetsa magazi a anthu,
Ndiponso unachitira chiwawa dziko lapansi,
Komanso mizinda ndi anthu onse okhala mmenemo.+