10 Mfumu ya Isiraeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anali atakhala pabwalo la pachipata cha Samariya. Aliyense anakhala pampando wake wachifumu atavala zovala zachifumu.+ Pamaso pawo panali aneneri onse ndipo anali kuchita zinthu monga mmene aneneri amachitira.+