13 “Iwe mwana wa munthu, ngati dziko landichimwira pochita zosakhulupirika,+ ndidzalitambasulira dzanja langa n’kuthyola ndodo zake zimene amakolowekapo mikate yoboola pakati.+ Komanso ndidzalitumizira njala+ ndipo ndidzapha anthu ndi ziweto m’dzikolo.”+