-
Yesaya 63:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Ndidzanena za ntchito za Yehova zosonyeza kukoma mtima kwake kosatha.+ Ndidzatamanda Yehova, mogwirizana ndi zonse zimene Yehova watichitira.+ Ndidzauza nyumba ya Isiraeli zabwino zochuluka+ zimene iye wawachitira chifukwa cha chifundo chake,+ komanso chifukwa cha kukoma mtima kwake kosatha ndiponso kwakukulu.
-
-
Yeremiya 31:12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Pamenepo iwo adzabwera ndi kufuula mosangalala pamwamba pa phiri la Ziyoni.+ Nkhope zawo zidzawala chifukwa cha ubwino wa Yehova.+ Zidzawalanso chifukwa cha mbewu, vinyo watsopano,+ mafuta, ana a nkhosa ndi ana a ng’ombe.+ Moyo wawo udzakhala ngati munda wothiriridwa bwino+ ndipo sadzakhalanso ofooka.”+
-