10 Chilichonse chimene maso anga anali kupempha sindinali kuwamana.+ Mtima wanga sindinaumane chosangalatsa cha mtundu uliwonse. Ndinasangalalanso ndi ntchito yonse imene ndinaigwira mwakhama.+ Imeneyi ndiyo inali mphoto yanga ya ntchito yonse imene ndinagwira mwakhama.+