11 Rehobowamu atafika ku Yerusalemu,+ nthawi yomweyo anasonkhanitsa amuna ochita kusankhidwa odziwa kumenya nkhondo okwanira 180,000+ a nyumba yonse ya Yuda ndi ya Benjamini.+ Anawasonkhanitsa kuti akamenyane ndi Isiraeli pofuna kuti ufumu ubwerere kwa Rehobowamu.