14 Choncho Hezekiya mfumu ya Yuda anatumiza uthenga kwa mfumu ya Asuri ku Lakisi, wakuti: “Ndachimwa. Siyani kundiukira. Ndikupatsani chilichonse chimene mungandilamule.”+ Chotero mfumu ya Asuri inalamula Hezekiya mfumu ya Yuda kuti apereke matalente 300 a siliva+ ndi matalente 30 a golide.