-
Yoswa 3:16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 madzi otsika kuchokera kumtunda anayamba kuima. Madziwo anakwera m’mwamba, ndipo anasefukira n’kupanga damu,+ limene linafika kutali kwambiri. Izi zinachitikira ku Adamu, mzinda woyandikana ndi mzinda wa Zeretani.+ Koma madzi omwe anali kutsikira kunyanja ya Araba, imene ndiyo Nyanja Yamchere,+ anaphwa. Choncho, madzi a mtsinjewo anaduka, ndipo anthuwo anawolokera kutsidya lina, pafupi ndi Yeriko.
-