20 Anthuwo ananyamuka m’mawa kwambiri n’kupita kuchipululu+ cha Tekowa.+ Ali m’njira, Yehosafati anaimirira n’kunena kuti: “Tamverani inu Ayuda ndi anthu okhala mu Yerusalemu!+ Khulupirirani+ Yehova Mulungu wanu kuti mukhalitse. Khulupirirani aneneri+ ake kuti zinthu zikuyendereni bwino.”