14 Koma wansembe Yehoyada anatenga atsogoleri a magulu a asilikali 100, kapena kuti asilikali osankhidwa, n’kuwauza kuti: “M’chotseni pakati pa mizere ya anthu!+ Aliyense amene angam’tsatire pambuyo pake aphedwe ndi lupanga!” Popeza wansembeyo anali atanena kuti: “Musam’phere panyumba ya Yehova.”