51 Pa mapeto pake, Mfumu Solomo inamaliza+ ntchito yonse yokhudza nyumba ya Yehova imene inayenera kugwira. Kenako Solomo anayamba kubweretsa zinthu zonse zimene Davide bambo ake+ anaziyeretsa. Anatenga siliva, golide, ndi ziwiya zina n’kukaziika mosungira chuma cha panyumba ya Yehova.+