17 Patapita nthawi, Ahaziya anamwalira,+ mogwirizana ndi mawu+ a Yehova amene Eliya ananena. Kenako Yehoramu+ anayamba kulamulira m’malo mwake chifukwa Ahaziya analibe mwana wamwamuna. Iye anayamba kulamulira m’chaka chachiwiri cha Yehoramu+ mwana wa Yehosafati mfumu ya Yuda.