Ekisodo 34:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Pakuti simuyenera kugwadira mulungu wina,+ chifukwa Yehova, amene dzina lake ndi Nsanje, alidi Mulungu wansanje.*+ Levitiko 26:30 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 30 Ndipo ndidzafafaniza malo anu opatulika olambirirako+ ndi kugwetsa maguwa anu ofukizirapo zonunkhira. Ndidzaponya mitembo yanu pamwamba pa mafano anu onyansa* opanda moyowo,+ ndipo mudzakhala onyansa kwa ine.+ 1 Mafumu 12:28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 Choncho mfumuyo inakambirana ndi anthu ena+ n’kupanga ana awiri a ng’ombe agolide.+ Itatero inauza anthuwo kuti: “N’zovuta kwambiri kwa inu kuti muzipita ku Yerusalemu. Nayu Mulungu wanu+ Aisiraeli inu, amene anakutulutsani m’dziko la Iguputo.”+ 1 Mafumu 21:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Ahabu anachita zinthu zonyansa kwambiri mwa kutsatira mafano onyansa+ monga momwe Aamori, amene Yehova anawathamangitsa pamaso pa ana a Isiraeli, anachitira.’”+
14 Pakuti simuyenera kugwadira mulungu wina,+ chifukwa Yehova, amene dzina lake ndi Nsanje, alidi Mulungu wansanje.*+
30 Ndipo ndidzafafaniza malo anu opatulika olambirirako+ ndi kugwetsa maguwa anu ofukizirapo zonunkhira. Ndidzaponya mitembo yanu pamwamba pa mafano anu onyansa* opanda moyowo,+ ndipo mudzakhala onyansa kwa ine.+
28 Choncho mfumuyo inakambirana ndi anthu ena+ n’kupanga ana awiri a ng’ombe agolide.+ Itatero inauza anthuwo kuti: “N’zovuta kwambiri kwa inu kuti muzipita ku Yerusalemu. Nayu Mulungu wanu+ Aisiraeli inu, amene anakutulutsani m’dziko la Iguputo.”+
26 Ahabu anachita zinthu zonyansa kwambiri mwa kutsatira mafano onyansa+ monga momwe Aamori, amene Yehova anawathamangitsa pamaso pa ana a Isiraeli, anachitira.’”+