-
1 Mafumu 13:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Ndiyeno anafuulira guwa lansembelo mawu ochokera kwa Yehova oitanira tsoka, kuti: “Guwa lansembe iwe! Guwa lansembe iwe! Yehova wanena kuti, ‘Mwana wamwamuna adzabadwa m’nyumba ya Davide, dzina lake Yosiya.+ Ndithu adzatenga ansembe a malo okwezeka amene akufukiza nsembe yautsi pa iwe, n’kuwapereka nsembe pa iwe. Iye adzawotcha mafupa a anthu pa iwe.’”+
-
-
2 Mafumu 23:8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Kenako inaitanitsa ansembe onse kuchokera m’mizinda ya Yuda. Inawaitanitsa kuti isandutse malo okwezeka kukhala osayenera kulambirako, kumene ansembewo ankafukizako nsembe yautsi, kuyambira ku Geba+ mpaka ku Beere-seba.+ Inagwetsa malo okwezeka a pazipata amene anali pakhomo la pachipata cha Yoswa mkulu wa mzindawo. Chipata cha Yoswacho chinali mbali ya kumanzere munthu akamalowa pachipata cha mzindawo.
-