Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mafumu 21:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Koma anthu a m’dzikolo anapha anthu onse amene anachitira chiwembu+ Mfumu Amoni. Kenako anthu a m’dzikolo anaika Yosiya+ mwana wake kuti akhale mfumu m’malo mwake.

  • 2 Mafumu 22:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Yosiya+ anali ndi zaka 8 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira zaka 31 ku Yerusalemu. Mayi ake anali a ku Bozikati.+ Dzina lawo linali Yedida mwana wa Adaya.

  • 2 Mafumu 23:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Komanso guwa lansembe limene linali ku Beteli+ ndi malo okwezeka amene Yerobowamu+ mwana wa Nebati amene anachimwitsa Isiraeli+ anamanga, ngakhale guwa lansembe limenelo ndi malo okwezekawo, mfumuyo inagumula. Kenako inatentha malo okwezekawo n’kuwaperapera mpaka kusanduka fumbi. Inatenthanso mzati wopatulika.

  • 2 Mafumu 23:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 M’masiku ake, Farao Neko+ mfumu ya Iguputo inabwera kudzathandiza mfumu ya Asuri pamtsinje wa Firate,+ ndipo Mfumu Yosiya inapita kukamenyana ndi mfumu ya Iguputoyo,+ koma mfumuyo inapha Yosiya+ ku Megido+ itangomuona.

  • 2 Mbiri 34:33
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 33 Atatero, Yosiya anachotsa zonyansa zonse+ m’mayiko onse a ana a Isiraeli.+ Anachititsanso anthu onse amene anali mu Isiraeli kuti ayambe kutumikira Yehova Mulungu wawo. M’masiku ake onse, iwo sanasiye kutsatira Yehova Mulungu wa makolo awo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena