25 Adamu anagonanso ndi mkazi wake Hava, ndipo mkaziyo anabereka mwana wamwamuna yemwe anamupatsa dzina lakuti Seti.+ Hava anapereka dzina limeneli chifukwa chakuti Seti atabadwa, Havayo ananena kuti: “Mulungu wandipatsa mbewu ina m’malo mwa Abele, popeza iye anaphedwa ndi Kaini.”+