16 Ndiyeno pamene likasa la Yehova linalowa mu Mzinda wa Davide, Mikala+ mwana wamkazi wa Sauli anasuzumira pawindo kuyang’ana pansi ndipo anaona Mfumu Davide akudumphadumpha ndi kuvina mozungulira pamaso pa Yehova. Pamenepo Mikala anayamba kum’peputsa+ mumtima mwake.+