46 Kenako Mose anauza Aroni kuti: “Tenga chofukizira uikemo moto wochokera paguwa lansembe.+ Uikemo nsembe yofukiza n’kupita kwa khamulo mofulumira kuti ukawaphimbire machimo awo.+ Chita zimenezi chifukwa Yehova wakwiya kwambiri.+ Mliritu wayamba kale!”