6 Patapita nthawi, mfumu ndi anthu ake anapita ku Yerusalemu kukamenyana ndi Ayebusi+ amene anali kukhala kumeneko. Ayebusiwo anayamba kuuza Davide kuti: “Sulowa mumzinda uno, pakuti upitikitsidwa ndi anthu akhungu ndi olumala.”+ Mumtima mwawo iwo anali kunena kuti: “Davide sangalowe mumzinda uno.”