5 Pogawapo, anachita maere+ panyumba ya Eleazara pamodzi ndi panyumba ya Itamara. Anachita zimenezi chifukwa chakuti panafunika atsogoleri a pamalo oyera,+ ndi atsogoleri otumikira Mulungu woona, ochokera mwa ana a Eleazara ndiponso ochokera mwa ana a Itamara.