15 Kenako anafika kwa mfumu, ndipo mfumuyo inamufunsa kuti: “Mikaya, kodi tipite kukamenyana ndi Ramoti-giliyadi, kapena tisapite?” Nthawi yomweyo Mikaya anayankha kuti: “Pitani mukapambana. Mosakayikira, Yehova akapereka mzindawo m’manja mwanu mfumu.”+