-
1 Mbiri 27:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Tsopano nawa magulu a Aisiraeli amene anali m’gulu la asilikali a mfumu. M’magulu amenewa munali atsogoleri a nyumba za makolo awo,+ atsogoleri+ a magulu a anthu 1,000, atsogoleri a magulu a anthu 100,+ ndi atsogoleri amene anali kusamalira magulu amenewa. Maguluwa anali kusinthanasinthana mwezi uliwonse pa chaka kutumikira+ mfumu, ndipo gulu lililonse linali ndi anthu 24,000.
-