25 Ndipo Mose anasankha amuna oyenerera mu Isiraeli yense ndi kuwapatsa udindo wokhala atsogoleri a anthu,+ kuti akhale atsogoleri a magulu a anthu 1,000, atsogoleri a magulu a anthu 100, atsogoleri a magulu a anthu 50 ndi atsogoleri a magulu a anthu 10.
12 Idzaika anthu ena kukhala atsogoleri a magulu a anthu 1,000+ ndi atsogoleri a magulu a anthu 50.+ Ena azidzalima minda yake+ ndi kukolola mbewu zake,+ ndiponso ena azidzapanga zida zake zankhondo+ ndi zida zogwiritsa ntchito pamagaleta ake.+
2 Tsopano Solomo anaitanitsa Aisiraeli onse, atsogoleri a magulu a anthu 1,000,+ atsogoleri a magulu a anthu 100,+ oweruza,+ ndi akuluakulu onse a Isiraeli+ yense, amene anali atsogoleri a nyumba za makolo awo.+