8 Akalonga ake+ anapereka nsembe yaufulu kwa anthuwo,+ kwa ansembe ndi kwa Alevi. Hilikiya,+ Zekariya ndi Yehiela monga atsogoleri a nyumba ya Mulungu woona, anapereka kwa ansembe nkhosa ndi mbuzi zokwana 2,600 ndiponso ng’ombe 300 kuti zikhale nyama zophera pasika.