Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 26:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 pamenepo ine ndidzakuchitani zotsatirazi: pokulangani ndidzakugwetserani zoopsa za chifuwa chachikulu+ ndi kuphwanya kwa thupi koopsa, kumene kudzachititsa maso anu khungu+ ndi kukufooketsani.+ Simudzapindula ndi mbewu zimene mwafesa, chifukwa adani anu adzadya zokolola zanuzo.+

  • Deuteronomo 28:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 “Mukapanda kumvera mawu a Yehova Mulungu wanu ndi kuonetsetsa kuti mukutsatira malamulo ake onse ndi mfundo zake zimene ndikukupatsani lero, matemberero otsatirawa adzakugwerani ndi kukupezani:+

  • Deuteronomo 30:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 ndikukuuzani lero kuti mudzatheratu.+ Simudzatalikitsa masiku anu panthaka imene mukupita kukaitenga kukhala yanu mutawoloka Yorodano.

  • Yoswa 23:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 dziwani kuti Yehova Mulungu wanu adzaleka kuwapitikitsa pamaso panu.+ Iwo adzakhala ngati msampha ndiponso ngati khwekhwe kwa inu.+ Adzakhalanso ngati zokubayani* m’mbali mwanu komanso ngati zitsotso m’maso mwanu, kufikira mutatheratu padziko labwinoli limene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.+

  • Danieli 9:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Anthu onse a mu Isiraeli aphwanya malamulo anu ndipo apatuka mwa kusamvera mawu anu.+ Choncho inu mwatitsanulira temberero ndi malumbiro+ amene analembedwa m’chilamulo cha Mose, mtumiki wa Mulungu woona, pakuti takuchimwirani.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena