29 Nthawi ndi nthawi anali kugula galeta lochokera ku Iguputo pamtengo wa ndalama zasiliva 600. Hatchi anali kuigula pamtengo wa ndalama zasiliva 150. Umu ndi mmene mafumu onse a Ahiti+ ndi mafumu a ku Siriya anali kuchitira. Mafumuwa ankagwiritsa ntchito amalondawo pogula zinthuzo.