-
Yobu 42:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Abale ake onse, alongo ake onse ndi onse amene anali kumudziwa kale+ ankabwera kwa iye. Iwo anayamba kudyera naye pamodzi mkate+ m’nyumba mwake, komanso anali kumulimbikitsa ndi kum’pepesa chifukwa cha tsoka lonse limene Yehova analola kuti lim’gwere. Aliyense wa iwo anapatsa Yobu mphatso ya ndalama ndi mphete yagolide.
-