14 Komanso, anthu ndi atsogoleri onse a ansembe+ anachita zosakhulupirika zochuluka kwambiri mofanana ndi zonyansa zonse+ za anthu a mitundu ina. Choncho iwo anaipitsa nyumba ya Yehova imene iye anaiyeretsa ku Yerusalemu.+
19 Amene apatuka pa panganoli ndi akalonga a Yuda, akalonga a Yerusalemu,+ nduna za panyumba ya mfumu, ansembe ndi anthu onse a m’dzikoli amene anadutsa pakati pa mwana wa ng’ombe wodulidwa pakatiyo . . .